25M’chaka cha 9+ cha ufumu wa Zedekiya, m’mwezi wa 10,+ pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera+ ku Yerusalemu pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo. Anabwera kudzachita nkhondo ndi mzindawo ndipo anamanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+
4 Ndiyeno m’chaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya,+ m’mwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadirezara mfumu ya Babulo pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwera ku Yerusalemu+ kudzaukira mzindawo. Atafika anayamba kumanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+