Yeremiya 1:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “Koma iwe umange m’chiuno+ ndipo upite kukawauza zonse zimene ndikulamule kuti ukawauze. Usagwidwe ndi mantha chifukwa cha iwo,+ kuopera kuti ndingakuchititse kugwidwa ndi mantha pamaso pawo. Yeremiya 26:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndiyeno Yeremiya atamaliza kulankhula mawu onse amene Yehova anamulamula kuti akauze anthu onse, nthawi yomweyo ansembe, aneneri ndi anthu onse anamugwira ndi kunena kuti: “Ukufa basi.+ Yeremiya 42:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ndiyeno iwo anauza Yeremiya kuti: “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika, ndipo atilange+ ngati sitidzachita ndendende mogwirizana ndi mawu onse amene Yehova Mulungu wako angakutume kwa ife.+
17 “Koma iwe umange m’chiuno+ ndipo upite kukawauza zonse zimene ndikulamule kuti ukawauze. Usagwidwe ndi mantha chifukwa cha iwo,+ kuopera kuti ndingakuchititse kugwidwa ndi mantha pamaso pawo.
8 Ndiyeno Yeremiya atamaliza kulankhula mawu onse amene Yehova anamulamula kuti akauze anthu onse, nthawi yomweyo ansembe, aneneri ndi anthu onse anamugwira ndi kunena kuti: “Ukufa basi.+
5 Ndiyeno iwo anauza Yeremiya kuti: “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika, ndipo atilange+ ngati sitidzachita ndendende mogwirizana ndi mawu onse amene Yehova Mulungu wako angakutume kwa ife.+