18 Kodi izi si zimene makolo anu anachita,+ mwakuti Mulungu wathu anadzetsa tsoka lonseli+ pa ife komanso pamzinda uwu? Koma inu mukuwonjezera kuyaka kwa mkwiyo wake pa Isiraeli mwa kuipitsa sabata.”+
11 Anthu onse a mu Isiraeli aphwanya malamulo anu ndipo apatuka mwa kusamvera mawu anu.+ Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro+ amene analembedwa m’chilamulo cha Mose, mtumiki wa Mulungu woona, pakuti takuchimwirani.