Miyambo 17:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+ Maliro 1:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Anthu amva mmene ndikuusira moyo ngati mkazi,+ koma palibe wonditonthoza.+Adani anga onse amva za tsoka+ langa. Iwo akondwera,+ chifukwa ndinu mwachititsa zimenezi.Inu mubweretsadi tsiku limene mwanena,+ kuti iwo akhale ngati ine.+ Obadiya 12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Iwe sunayenera kumangoonerera mosangalala pa tsiku limene m’bale wako anakumana ndi tsoka.+ Sunayenera kusangalala pa tsiku limene ana a Yuda anali kuwonongedwa.+ Sunayeneranso kulankhula modzitama pa tsiku limene iwo anamva zowawa.
5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+
21 Anthu amva mmene ndikuusira moyo ngati mkazi,+ koma palibe wonditonthoza.+Adani anga onse amva za tsoka+ langa. Iwo akondwera,+ chifukwa ndinu mwachititsa zimenezi.Inu mubweretsadi tsiku limene mwanena,+ kuti iwo akhale ngati ine.+
12 “Iwe sunayenera kumangoonerera mosangalala pa tsiku limene m’bale wako anakumana ndi tsoka.+ Sunayenera kusangalala pa tsiku limene ana a Yuda anali kuwonongedwa.+ Sunayeneranso kulankhula modzitama pa tsiku limene iwo anamva zowawa.