Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 29:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Pamenepo anthu adzanena kuti, ‘N’chifukwa chakuti anataya pangano+ la Yehova Mulungu wa makolo awo, limene anapangana nawo pamene anali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo.+

  • Oweruza 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ n’kuyamba kutsatira milungu ina mwa milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milungu imeneyo, moti anakhumudwitsa Yehova.+

  • Nehemiya 9:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “Koma iwo anakhala osamvera+ ndipo anakupandukirani.+ Anapitiriza kufulatira chilamulo chanu,+ ndipo anapha aneneri anu+ amene anali kuwalimbikitsa kuti abwerere kwa inu.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani.+

  • Yeremiya 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ansembe sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova?’+ Ndipo anthu ophunzitsa chilamulo sanandidziwe.+ Abusa nawonso anaphwanya malamulo anga,+ ndipo aneneri anali kulosera m’dzina la Baala+ ndi kutsatira milungu yopanda phindu.+

  • Yeremiya 5:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kodi ndingakukhululukire bwanji zinthu zimenezi? Ana ako aamuna andisiya ndipo amalumbira+ pa zinthu zina osati Mulungu.+ Ndinali kuwapatsa zofuna zawo+ koma anapitiriza kuchita chigololo+ ndipo anali kupita kunyumba ya hule m’magulumagulu.

  • Yeremiya 22:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndipo adzanena kuti: “Anauchitira zimenezi chifukwa chakuti anthu a mumzindawu anasiya pangano la Yehova Mulungu wawo+ ndi kuyamba kulambira milungu ina ndi kuitumikira.”’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena