Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 55:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+

  • Yeremiya 7:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Iwo amanga malo okwezeka ku Tofeti,+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ kuti azitentha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuchita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’+

  • Yeremiya 18:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 ndiyeno anthuwo n’kusiya zoipa zimene anali kuchita, zimene ndinawadzudzula nazo,+ pamenepo ndidzasintha maganizo anga kuti ndisawagwetsere tsoka limene ndinafuna kuwagwetsera.+

  • Ezekieli 33:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Auze kuti, ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa,+ koma ndimafuna kuti munthu woipa abwerere+ kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo.+ Bwererani! Bwererani ndi kusiya njira zanu zoipa.+ Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?”’+

  • Aheberi 12:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakuti bambo athu otiberekawo, kwa masiku ochepa anali kutilanga malinga ndi zimene anaziona kuti n’zoyenera,+ koma Mulungu amatilanga kuti tipindule ndiponso kuti tikhale oyera ngati iyeyo.+

  • Yakobo 1:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Munthu akakhala pa mayesero+ asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.

  • 2 Petulo 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake,+ ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena