Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Pakuti pa kukwiya kwanga moto wayaka,+

      Ndipo udzayaka mpaka kukafika ku Manda,* malo a pansi penipeni.+

      Udzanyeketsa dziko lapansi ndi zipatso zake,+

      Ndi kuyatsa maziko a mapiri.+

  • 2 Mafumu 25:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu,+ nyumba zonse za mu Yerusalemu,+ ndi nyumba ya munthu aliyense wotchuka.+

  • Salimo 89:46
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 46 Inu Yehova, kodi mudzadzibisa kufikira liti? Ku nthawi zonse?+

      Kodi mkwiyo wanu udzakhalabe ukuyaka ngati moto?+

  • Yesaya 42:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Choncho Mulungu anali kuwakhuthulira mkwiyo, ukali wake, ndi nkhondo yoopsa.+ Nkhondoyo inali kuwapsereza+ koma iwo sanazindikire.+ Inapitiriza kuwatentha koma iwo sanaganizire chilichonse mumtima mwawo.+

  • Yeremiya 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Chitani mdulidwe wa mitima yanu pamaso pa Yehova,+ inu anthu a ku Yuda ndi okhala mu Yerusalemu. Chitani zimenezi kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto, pakuti ukatero udzayaka popanda munthu wozimitsa, chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+

  • Yeremiya 7:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani! Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zikutsanulidwa pamalo awa,+ pamunthu, pachiweto, pamtengo wakuthengo,+ ndi pachipatso chilichonse chochokera m’nthaka yawo, ndipo udzayaka moti sudzazimitsidwa.’+

  • Maliro 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova wasonyeza ukali wake wonse.+ Wakhuthula mkwiyo wake woyaka moto.+

      Iye wayatsa moto m’Ziyoni, umene wanyeketsa maziko ake.+

  • Aheberi 12:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Pakuti Mulungu wathu alinso moto wowononga.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena