Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 18:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Zimene zichitike n’zakuti ine ndikasiyana nanu, mzimu+ wa Yehova ubwera n’kukutengani kupita nanu kwina kumene ine sindikukudziwa. Ineyo ndikhala nditamuuza kale Ahabu, koma iyeyo sadzakupezani choncho adzandipha ndithu.+ Komatu mtumiki wanune ndakhala ndikuopa Yehova kuyambira ubwana wanga.+

  • 2 Mafumu 2:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndiyeno ana a aneneriwo anauza Elisa kuti: “Ife atumiki anu tili ndi amuna 50 amphamvu, bwanji tiwatume kukafunafuna mbuye wanu? Mwina mzimu+ wa Yehova wamunyamula ndipo wam’ponya paphiri linalake kapena m’chigwa.” Koma Elisa anayankha kuti: “Ayi musawatumize.”

  • Ezekieli 8:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Kenako iye anatambasula chinachake chooneka ngati dzanja+ ndipo anagwira tsitsi la kumutu kwanga n’kundinyamula. Ndiyeno mzimu+ unandinyamulira m’malere, pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, n’kundipititsa ku Yerusalemu m’masomphenya a Mulungu.+ Unandifikitsa pakhomo la kanyumba ka pachipata cha bwalo lamkati+ choyang’ana kumpoto. Pamenepo m’pamene panali kukhala chizindikiro choimira nsanje, chimene chinali kuchititsa Mulungu nsanje.+

  • Machitidwe 8:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Atatuluka m’madzimo, mzimu wa Yehova unachotsa Filipo mwamsanga pamalopo,+ ndipo nduna ija sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena