-
1 Mafumu 5:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Antchito anga adzainyamula ku Lebanoni+ n’kutsikira nayo kunyanja, ndipo ineyo kumbali yanga ndidzaimanga pamodzi ngati phaka n’kuiyandamitsa panyanja kuti ikafike kumalo kumene mudzandiuze.+ Kenako ndidzauza anthu kuti aimasule, ndipo inuyo mukaitengera kumeneko. Ndipo inu mudzachita zofuna zanga pondipatsa chakudya cha banja langa.”+
-
-
Ezara 3:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kenako anthuwo anapereka ndalama+ kwa anthu osema miyala+ ndi kwa amisiri,+ ndiponso anapereka chakudya,+ zakumwa ndi mafuta+ kwa Asidoni+ ndi kwa anthu a ku Turo,+ kuti abweretse matabwa a mkungudza kuchokera ku Lebanoni+ n’kudzawasiya m’mphepete mwa nyanja ku Yopa.+ Anachita zimenezi malinga ndi chilolezo chimene Koresi+ mfumu ya ku Perisiya anawapatsa.
-
-
Machitidwe 12:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Tsopano Herode anali wokwiya ndi anthu a ku Turo ndi ku Sidoni, ndipo anafuna kuwathira nkhondo. Choncho onse anabwera kwa iye mogwirizana. Ndipo iwo atanyengerera Balasito, amene anali woyang’anira chipinda chogona cha mfumu, anayamba kupempha mtendere. Iwo anachita zimenezi chifukwa dziko lawo linali kudalira chakudya+ chochokera m’dziko la mfumuyo.
-