5 Pamenepo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova ndikadzatambasula dzanja langa ndi kukantha Iguputo.+ Motero ndidzatulutsa ana a Isiraeli m’dzikolo.”+
12 Dziko la Iguputo ndidzalisandutsa bwinja pakati pa mayiko omwe simukukhalanso anthu.+ Kwa zaka 40, mizinda yake idzakhala mabwinja pakati pa mizinda yopanda anthu.+ Ndidzamwaza Aiguputo pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira m’mayiko ena.”+
19 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndipereka dziko la Iguputo kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo.+ Adzatenga chuma chake chochuluka ndi kulanda zinthu zake zambiri.+ Zimenezi zidzakhala malipiro a gulu lake lankhondo.’