Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Pamenepo udzakhala chodabwitsa,+ adzakupekera mwambi+ ndi kukutonza pakati pa mitundu yonse ya anthu amene Yehova adzakupititsako.

  • Salimo 44:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Mwatisandutsa chitonzo kwa anthu oyandikana nafe,+

      Mwatisandutsa chinthu chonyozeka ndi choseketsa kwa onse otizungulira.+

  • Yeremiya 18:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Choncho dziko lawo lidzakhala chinthu chodabwitsa kwa ena,+ chinthu chimene adzachiimbira mluzu mpaka kalekale.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi dzikoli adzaliyang’anitsitsa modabwa ndipo adzapukusa mutu wake.+

  • Maliro 2:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Anthu onse odutsa mumsewu akakuona, akuwomba m’manja+ monyodola.

      Akuimba mluzu+ ndi kupukusa mitu+ yawo poona mwana wamkazi wa Yerusalemu. Iwo akunena kuti:

      “Kodi uwu ndi mzinda umene anali kunena kuti, ‘Ndi wokongola kwambiri, wotamandika padziko lonse lapansi’?”+

  • Danieli 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera.+ Pakuti chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu,+ Yerusalemu ndi anthu anu takhala chinthu chotonzedwa ndi anthu onse otizungulira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena