5Ndikufuna ndimuimbire nyimbo munthu amene ndimamukonda. Imeneyi ndi nyimbo yonena za munthu amene ndimamukonda, ndiponso munda wake wa mpesa.+ Wokondedwa wanga anali ndi munda wa mpesa pamalo achonde m’mbali mwa phiri.
2 “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wa mpesa+ umasiyana bwanji ndi mitengo ina yonse? Kodi kamtengo kophuka pambali pa mtengowo pakati pa mitengo ya m’nkhalango kamasiyana bwanji ndi mitengo ina?