-
Danieli 7:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 “Kenako ndinaonanso m’masomphenya ausiku chilombo chachinayi, choopsa kwambiri ndiponso chochititsa mantha komanso champhamvu kwambiri.+ Chinali ndi mano akuluakulu achitsulo ndipo chinali kudya ndi kuphwanyaphwanya chilichonse chimene chinali nacho pafupi. Zotsala chinali kuzipondaponda ndi mapazi ake. Chinali chosiyana ndi zilombo zina zonse zimene ndinaona poyamba ndipo chinali ndi nyanga 10.+
-
-
Danieli 7:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 “Ndiyeno ndinali ndi chidwi chofuna kudziwa zambiri zokhudza chilombo chachinayi chija, chimene chinali chosiyana ndi zina zonse. Chilombo chimenechi chinali choopsa kwambiri. Mano ake anali achitsulo, zikhadabo zake zinali zamkuwa, ndipo chinali kudya zinthu ndi kuziphwanyaphwanya. Zotsala chinali kuzipondaponda ndi mapazi ake.+
-