Mateyu 3:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Inetu ndikukubatizani m’madzi+ chifukwa cha kulapa kwanu,+ koma amene akubwera+ m’mbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindili woyenera kumuvula nsapato zake.+ Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyera+ komanso ndi moto.+ Maliko 1:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ine ndakubatizani ndi madzi, koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.”+ Machitidwe 2:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana,+ monga mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.
11 Inetu ndikukubatizani m’madzi+ chifukwa cha kulapa kwanu,+ koma amene akubwera+ m’mbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindili woyenera kumuvula nsapato zake.+ Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyera+ komanso ndi moto.+
4 Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana,+ monga mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.