Ekisodo 20:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu.+ Musagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo wokhala mumzinda wanu.+ Nehemiya 13:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Ndiyeno mdima utafika pazipata za Yerusalemu, sabata lisanayambe, ndinapereka lamulo ndipo zitseko zinayamba kutsekedwa.+ Ndinalamulanso kuti asatsegule zitsekozo kufikira sabata litatha. Ndipo ndinaika ena mwa atumiki anga m’zipata kuti munthu asalowe ndi katundu tsiku la sabata.+ Yeremiya 17:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Yehova wanena kuti: “Samalani moyo wanu.+ Katundu aliyense amene mukufuna kulowa naye pazipata za Yerusalemu musamunyamule pa tsiku la sabata.+ Mateyu 12:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Afarisi ataona zimenezi anamuuza kuti:+ “Taona! Ophunzira ako akuchita zosayenera kuzichita pa sabata.”+ Luka 6:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Afarisi ena ataona zimenezi anati: “N’chifukwa chiyani mukuchita zosemphana ndi malamulo+ pa sabata?”+
10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu.+ Musagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo wokhala mumzinda wanu.+
19 Ndiyeno mdima utafika pazipata za Yerusalemu, sabata lisanayambe, ndinapereka lamulo ndipo zitseko zinayamba kutsekedwa.+ Ndinalamulanso kuti asatsegule zitsekozo kufikira sabata litatha. Ndipo ndinaika ena mwa atumiki anga m’zipata kuti munthu asalowe ndi katundu tsiku la sabata.+
21 Yehova wanena kuti: “Samalani moyo wanu.+ Katundu aliyense amene mukufuna kulowa naye pazipata za Yerusalemu musamunyamule pa tsiku la sabata.+
2 Afarisi ataona zimenezi anamuuza kuti:+ “Taona! Ophunzira ako akuchita zosayenera kuzichita pa sabata.”+
2 Afarisi ena ataona zimenezi anati: “N’chifukwa chiyani mukuchita zosemphana ndi malamulo+ pa sabata?”+