17 Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa akuluakulu a Ayuda. Atasonkhana pamodzi, anawauza kuti: “Amuna inu, abale anga, ngakhale kuti sindinachite kanthu kotsutsana ndi anthu kapena mwambo wa makolo athu,+ ndinagwidwa mu Yerusalemu ndi kuperekedwa m’manja mwa Aroma monga mkaidi.+