5 Ndipotu mkulu wa ansembe ndi bungwe lonse la akulu+ angandichitire umboni. Kwa amenewa n’kumene ndinapezanso makalata+ opita kwa abale ku Damasiko. Ndinanyamuka kuti ndikagwire okhala kumeneko ndi kuwabweretsa ku Yerusalemu ali omangidwa kuti adzapatsidwe chilango.