1Ine Paulo ndili pamodzi ndi Timoteyo monga akapolo+ a Khristu Yesu. Ndikulembera oyera onse ogwirizana ndi Khristu Yesu amene ali ku Filipi,+ komanso oyang’anira ndi atumiki othandiza:+
2 Koma mukudziwa kuti choyamba titavutika+ ndi kuchitidwa zachipongwe+ ku Filipi,+ tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula+ kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.