Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 49:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+

  • Deuteronomo 18:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati panu, kuchokera pakati pa abale anu, ndipo inu mudzamvere mneneri ameneyo.+

  • Salimo 16:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakuti simudzasiya moyo wanga m’Manda.+

      Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.+

  • Yesaya 7:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Choncho Yehovayo akupatsani chizindikiro anthu inu: Tamverani! Mtsikana+ adzatenga pakati+ ndipo adzabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli.

  • Mika 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+

  • Malaki 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Taonani! Ine nditumiza mthenga wanga+ ndipo iye adzandikonzera njira.+ Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi+ Wake.+ Adzabwera ndi mthenga+ wa pangano+ amene mukumuyembekezera mosangalala.+ Iye adzabwera ndithu,” watero Yehova wa makamu.+

  • Machitidwe 9:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Koma Saulo anapitiriza kupeza mphamvu zambiri, ndipo anali kuthetsa nzeru Ayuda okhala mu Damasiko powafotokozera mfundo zomveka zotsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena