Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 49:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+

  • Numeri 24:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndidzamuona,+ koma si nthawi ino;

      Ndidzam’penya, koma si panopo.

      Ndithu nyenyezi+ idzatuluka mwa Yakobo,

      Ndodo yachifumu idzatulukadi mu Isiraeli.+

      Ndipo iye adzaphwanya chipumi cha Mowabu+

      Ndi chigaza cha ana onse ankhondo.

  • Luka 7:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Zitatero anthu onse anagwidwa ndi mantha,+ moti anayamba kutamanda Mulungu, kuti: “Mneneri wamkulu+ waonekera pakati pathu.” Analinso kunena kuti, “Mulungu wacheukira anthu ake.”+

  • Luka 24:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Iye anawafunsa kuti: “Zinthu zotani?” Iwo anamuuza kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti,+ amene anali mneneri+ wamphamvu m’ntchito ndi m’mawu pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.

  • Yohane 1:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Kenako Filipo anapeza Natanayeli+ n’kumuuza kuti: “Uja amene Mose analemba za iye m’Chilamulo+ komanso wotchulidwa m’Zolemba za aneneri,+ ife tam’peza. Iyeyu ndi Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti.”

  • Yohane 6:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Tsopano anthuwo ataona zizindikiro zimene anachitazo, anayamba kunena kuti: “Mosakayika uyu ndi mneneri+ uja amene anati adzabwera padziko.”

  • Machitidwe 3:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ndipotu Mose ananena kuti, ‘Yehova Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine kuchokera pakati pa abale anu.+ Mudzamumvere pa zinthu zonse zimene adzakuuzeni.+

  • Machitidwe 7:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 “Ameneyu ndi Mose amene anauza ana a Isiraeli kuti, ‘Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati pa abale anu.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena