Miyambo 15:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo,+ koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+ Agalatiya 6:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika+ mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu,+ yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale,+ kuopera kuti iyenso angayesedwe.+ Aefeso 4:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Muziyenda modzichepetsa nthawi zonse,+ mofatsa, moleza mtima,+ ndiponso mololerana m’chikondi.+ 1 Timoteyo 6:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi.+ M’malomwake tsatira chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa.+ 2 Timoteyo 2:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 ndi wolangiza mofatsa anthu otsutsa+ kuti mwina Mulungu angawalole kulapa,+ kuti adziwe choonadi molondola.+ 1 Petulo 3:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Koma vomerezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera.+ Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha+ aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.
6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika+ mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu,+ yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale,+ kuopera kuti iyenso angayesedwe.+
11 Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi.+ M’malomwake tsatira chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa.+
25 ndi wolangiza mofatsa anthu otsutsa+ kuti mwina Mulungu angawalole kulapa,+ kuti adziwe choonadi molondola.+
15 Koma vomerezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera.+ Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha+ aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.