Aefeso
4 Chotero ine, amene ndili m’ndende+ chifukwa cha Ambuye, ndikukuchondererani kuti muziyenda moyenera+ kuitana kumene munaitanidwa nako.+ 2 Muziyenda modzichepetsa nthawi zonse,+ mofatsa, moleza mtima,+ ndiponso mololerana m’chikondi.+ 3 Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa. Umodziwo timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.+ 4 Pali thupi limodzi+ ndi mzimu umodzi,+ mogwirizana ndi chiyembekezo chimodzi+ chimene munaitanidwira. 5 Palinso Ambuye mmodzi,+ chikhulupiriro chimodzi,+ ubatizo umodzi,+ 6 ndi Mulungu mmodzi+ amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse ndipo amachita zinthu kudzera mwa onse ndiponso mphamvu yake imagwira ntchito mwa onse.
7 Tsopano aliyense wa ife anapatsidwa kukoma mtima kwakukulu+ malinga ndi mmene Khristu anamuyezera mphatso yaulereyi.+ 8 Chotero iye anati: “Atakwera kumwamba anagwira anthu ukapolo ndipo anapereka mphatso za amuna.”+ 9 Tsopano, kodi mawu akuti “anakwera kumwamba”+ amatanthauza chiyani? Amatanthauza kuti anayamba watsika pansi, padziko.+ 10 Amene anatsikayo ndi amenenso anakwera+ kukakhala pamwambamwamba pa kumwamba konse,+ kuti adzazitse+ zinthu zonse.
11 Ndipo anapereka ena monga atumwi,+ ena monga aneneri,+ ena monga alaliki,*+ ena monga abusa ndi aphunzitsi,+ 12 kuti awongolere oyerawo,+ achite ntchito yotumikira, amange thupi la Khristu,+ 13 kufikira tonse tidzafike pa umodzi m’chikhulupiriro komanso pa kumudziwa molondola Mwana wa Mulungu, inde, kufikira tidzakhale munthu wachikulire,+ wofika pa msinkhu wauchikulire umene Khristu anafikapo.+ 14 Inde, kuti tisakhalenso tiana, otengekatengeka+ ngati kuti tikukankhidwa ndi mafunde, ndiponso otengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso+ chonyenga+ cha anthu, mwa kuchenjera kwa anthu popeka mabodza. 15 Koma polankhula zoona,+ tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi,+ pansi pa iye amene ndi mutu,+ Khristu. 16 Kuchokera kwa iye, thupi lonselo+ limakula podzimanga lokha mwachikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwirizana mwa mfundo iliyonse yogwira ntchito yake yofunikira, malinga ndi ntchito yoyenerera ya chiwalo chilichonse.+
17 Choncho, ndikunena izi ndi kuzichitira umboni mwa Ambuye, kuti musamayendenso monga mmene anthu a mitundu ina+ amayendera, potsatira maganizo awo opanda pake.+ 18 Pamene akuyenda motero, alinso mu mdima wa maganizo,+ otalikirana+ ndi moyo wa Mulungu, chifukwa cha umbuli+ umene uli mwa iwo, chifukwanso cha kukakala+ kwa mitima yawo. 19 Popeza iwo tsopano sakuthanso kuzindikira makhalidwe abwino,+ anadzipereka okha ku khalidwe lotayirira+ kuti achite chonyansa+ chamtundu uliwonse mwadyera.+
20 Koma inu simunaphunzire Khristu kukhala wotero,+ 21 malinga ngati munamumvadi. Ndiponso, monga mmene choonadi+ chilili mwa Yesu, munaphunzitsidwa mwa iye,+ 22 kuti muvule umunthu wakale+ umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale, umenenso ukuipitsidwa+ malinga ndi zilakolako zonyenga za umunthuwo.+ 23 Ndipo munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu,+ 24 ndi kuvala+ umunthu watsopano+ umene unalengedwa+ mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni+ ndi pa kukhulupirika.
25 Chotero, popeza tsopano mwataya chinyengo,+ aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnzake,+ chifukwa ndife ziwalo za thupi limodzi.+ 26 Kwiyani, koma musachimwe.+ Dzuwa lisalowe muli chikwiyire,+ 27 ndipo musam’patse malo Mdyerekezi.+ 28 Wakubayo asabenso,+ koma agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino,+ kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.+ 29 Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu,+ koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.+ 30 Komanso, musamamvetse chisoni mzimu woyera wa Mulungu,+ umene mwaikidwa chidindo chake,+ cha pa tsiku limene mudzamasulidwa ndi dipo.+
31 Kuwawidwa mtima konse kwa njiru,+ kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe+ zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.+ 32 Koma khalani okomerana mtima,+ achifundo chachikulu,+ okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso Mulungu anakukhululukirani ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.+