15 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati samva chisoni ngati mkwatiyo+ ali nawo limodzi, si choncho kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa+ pakati pawo, ndipo pa nthawiyo adzasala kudya.+
29 Iye amene ali ndi mkwatibwi ndiye mkwati.+ Koma mnzake wa mkwati, akaimirira ndi kumvetsera zimene akunena, amakhala n’chimwemwe chochuluka chifukwa cha mawu a mkwatiyo. Choncho chimwemwe changa chasefukiradi.+