14 Choncho Mawu ameneyo anakhala ndi thupi+ la nyama ndi kukhala pakati pathu, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wa mwana wobadwa yekha+ kwa bambo ake. Anali wodzaza ndi kukoma mtima kwakukulu ndi choonadi.+
14 “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Laodikaya,+ lemba kuti: Izi ndi zimene akunena Ame,+ mboni+ yokhulupirika+ ndi yoona,+ woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.+