Yohane
1 Pa chiyambi,+ panali wina wotchedwa Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu,+ komanso Mawuyo anali mulungu.*+ 2 Ameneyu anali ndi Mulungu+ pa chiyambi.+ 3 Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye,+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.
4 Moyo unakhalapo kudzera mwa iye,+ ndipo moyowo unali kuwala+ kounikira anthu. 5 Kuwalako kukuunika mumdima,+ ndipo mdimawo sunagonjetse kuwalako.
6 Panaonekera munthu wina amene anatumidwa monga nthumwi ya Mulungu.+ Dzina lake anali Yohane.+ 7 Munthu ameneyu anabwera monga mboni,+ kudzachitira umboni za kuwala,+ kuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye.+ 8 Sikuti iyeyu anali kuwalako ayi,+ koma anangobwera kudzachitira umboni+ za kuwalako.
9 Kuwala+ kwenikweni kumene kumaunikira+ anthu osiyanasiyana+ kunali pafupi kubwera m’dziko. 10 Iye anali m’dziko,+ ndipo dziko linakhalapo kudzera mwa iye.+ Koma dzikolo silinamudziwe. 11 Anabwera kudziko lakwawo, koma anthu akwawo enieniwo sanamulandire.+ 12 Komabe onse amene anamulandira,+ anawapatsa mphamvu zokhala ana a Mulungu,+ chifukwa amenewa anakhulupirira m’dzina lake.+ 13 Iwowa anabadwa kwa Mulungu, osati kudzera m’magazi kapena m’chifuniro cha thupi, kapena chifuniro cha anthu.+
14 Choncho Mawu ameneyo anakhala ndi thupi+ la nyama ndi kukhala pakati pathu, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wa mwana wobadwa yekha+ kwa bambo ake. Anali wodzaza ndi kukoma mtima kwakukulu ndi choonadi.+ 15 (Yohane anachitira umboni za iye, moti anali kuchita kufuula kuti: “Amene akubwera m’mbuyo mwangamu wandipitirira ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.”)+ 16 Pakuti tonsefe tinalandira zinthu kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo.+ Tinalandira kukoma mtima kwakukulu kosefukira.+ 17 Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi+ zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu. 18 Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse,+ mulungu wobadwa yekha+ amene ali pachifuwa+ cha Atate ndiye amene anafotokoza za Mulungu.+
19 Tsopano, Yohane anapereka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kuchokera ku Yerusalemu kukamufunsa kuti: “Kodi iwe ndiwe ndani?”+ 20 Iye anavomereza osakana ayi. Anavomereza ndithu, kuti: “Ine sindine Khristu ayi.”+ 21 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”+ Koma iye anati: “Iyayi.” “Kapena ndiwe Mneneri?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi!” 22 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Ndiwe ndani nanga? Tikufuna kudziwa kuti tikathe kupereka yankho kwa amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe ndani?”+ 23 Iye anati: “Ndine mawu a winawake wofuula m’chipululu kuti, ‘Wongolani njira ya Yehova,’ monga mmene mneneri Yesaya ananenera.”+ 24 Otumidwawo anachokera kwa Afarisi. 25 Choncho anamufunsa kuti: “Ngati iweyo sindiwe Khristu, kapena Eliya, kapenanso Mneneri, nanga n’chifukwa chiyani umabatiza anthu?”+ 26 Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza m’madzi. Pakati panu+ paimirira wina amene inu simukumudziwa.+ 27 Iye ndiye amene akubwera m’mbuyo mwangamu. Komabe, zingwe za nsapato zake ine sindili woyenera kuzimasula.”+ 28 Izi zinachitikira ku Betaniya wa kutsidya lina la Yorodano, kumene Yohane anali kubatiza anthu.+
29 Tsiku lotsatira anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu amene akuchotsa uchimo+ wa dziko!+ 30 Uyu ndi amene ndinali kunena uja kuti, M’mbuyo mwanga mukubwera munthu wina amene wandipitirira ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.+ 31 Inenso sindinali kumudziwa, koma chimene ndikubatizira anthu m’madzi n’chakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.”+ 32 Yohane anachitiranso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba, ndipo unakhalabe pa iye.+ 33 Inenso sindinali kumudziwa, koma Amene anandituma+ kudzabatiza m’madzi anandiuza kuti, ‘Ukadzaona mzimu ukutsika ndi kukhazikika pa munthu wina, ameneyo ndiye wobatiza ndi mzimu woyera.’+ 34 Ndipo ine ndaonadi zimenezo, ndachitira umboni ndithu kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”+
35 Tsiku lotsatiranso Yohane anaimirira ndi ophunzira ake awiri. 36 Poyang’anitsitsa Yesu akuyenda iye anati: “Onani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu!” 37 Ophunzira awiriwo anamumva akulankhula, ndipo anatsatira Yesu. 38 Pamenepo Yesu anacheuka. Atawaona akumutsatira, anawafunsa kuti: “Kodi mukufunafuna chiyani?” Iwo anati: “Rabi, (dzina lotanthauza, Mphunzitsi, polimasulira,) kodi mukukhala kuti?” 39 Iye anati: “Tiyeni mukaoneko.”+ Choncho anapita ndi kukaona kumene anali kukhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Pamenepo n’kuti nthawi ili cha m’ma 4 koloko madzulo.* 40 Andireya+ m’bale wake wa Simoni Petulo, anali mmodzi wa awiriwo amene anamva zimene Yohane ananena ndi kutsatira Yesu. 41 Choyamba iyeyu anapeza m’bale wake Simoni, ndi kumuuza kuti: “Ifetu tapeza Mesiya”+ (dzina lotanthauza, Khristu,+ polimasulira). 42 Kenako iye anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuyang’ana+ anati: “Iwe ndiwe Simoni+ mwana wa Yohane,+ udzatchedwa Kefa” (dzina limene kumasulira kwake ndi Petulo).+
43 Tsiku lotsatira, Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Ndiyeno anapeza Filipo+ n’kumuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+ 44 Filipo anali wochokera ku Betsaida,+ mumzinda wa Andireya ndi Petulo. 45 Kenako Filipo anapeza Natanayeli+ n’kumuuza kuti: “Uja amene Mose analemba za iye m’Chilamulo+ komanso wotchulidwa m’Zolemba za aneneri,+ ife tam’peza. Iyeyu ndi Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti.” 46 Koma Natanayeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?”+ Pamenepo Filipo anati: “Tiye ukaone.” 47 Yesu ataona Natanayeli akubwera momulunjika anati: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.”+ 48 Natanayeli anati: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ine ndinakuona, muja unali pansi pa mkuyu paja.” 49 Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinudi Mwana wa Mulungu,+ ndinu Mfumu+ ya Isiraeli.” 50 Poyankha Yesu anati: “Kodi wakhulupirira chifukwa ndakuuza kuti ndinakuona uli pansi pa mkuyu? Udzaona zazikulu kuposa izi.” 51 Anamuuzanso kuti: “Ndithudi ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, angelo+ a Mulungu akukwera ndi kutsikira kwa Mwana wa munthu.”+