Masalimo 117 Tamandani Yehova, inu mitundu yonse ya anthu.+Mulemekezeni, inu mafuko onse.+ 2 Pakuti kukoma mtima kosatha kumene watisonyeza ndi kwakukulu.+Ndipo choonadi+ cha Yehova chidzakhalapobe mpaka kalekale.Tamandani Ya, anthu inu!+