Nyimbo ya Davide pamene anali kuthawa mwana wake Abisalomu.+
3 Inu Yehova, n’chifukwa chiyani adani anga achuluka chotere?+
N’chifukwa chiyani anthu ondiukira achuluka?+
2 Ponena za moyo wanga, ambiri akuti:
“Mulungu sam’pulumutsa ameneyu.”+ [Seʹlah.]
3 Koma inu Yehova ndinu chishango changa,+
Ulemerero wanga+ ndiponso Wonditukula mutu.+
4 Ndidzafuulira Yehova mokweza,
Ndipo iye adzandiyankha m’phiri lake loyera.+ [Seʹlah.]
5 Koma ine ndidzagona pansi ndi kupeza tulo.
Ndidzadzuka ndithu, pakuti Yehova amandithandiza.+
6 Sindidzaopa anthu masauzande makumimakumi
Amene andiukira ndi kundizungulira.+
7 Nyamukani,+ inu Yehova! Ndipulumutseni+ inu Mulungu wanga!+
Pakuti mudzakantha adani anga onse pachibwano.+
Mano a anthu oipa mudzawaphwanyaphwanya.+
8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.+
Madalitso anu ali pa anthu anu.+ [Seʹlah.]