Yobu
26 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Koma ndiyetu wathandiza munthu wopanda mphamvu!
Ukuona ngati wapulumutsa dzanja lopanda nyonga,+
3 Walangiza munthu wopanda nzeru.+
Komanso ukuona ngati anthu ochuluka wawadziwitsa nzeru zopindulitsa.
4 Kodi wauza ndani mawu ako,
Ndipo zimene ukunenazi zachokera kuti?
7 Iye anatambasula kumpoto pamwamba pa malo opanda kanthu,+
Ndipo anakoloweka dziko lapansi m’malere.
8 Iye anakulunga madzi m’mitambo yake,+
Moti mitamboyo sing’ambika pansi pa madziwo.
9 Anaphimba mpando wake wachifumu,
Poukuta ndi mtambo wake.+
11 Zipilala za kumwamba zimagwedezeka,
Ndipo zimadabwa chifukwa cha kudzudzula kwake.