Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Duwa la Chikumbutso. Mikitamu.* Salimo la Davide. Nyimbo yophunzitsira.+ Pa nthawi imene Davide anali pankhondo ndi Aramu-naharaimu ndi Aramu-Zoba, ndipo Yowabu anabwerera ndi kukapha Aedomu 12,000 m’chigwa cha Mchere.+
60 Inu Mulungu, mwatitaya, ndipo mwasokoneza magulu athu ankhondo,+
Mwakwiya. Tiloleni tibwerere kwa inu.+
6 Pokhala woyera, Mulungu walankhula kuti:+
“Ndidzakondwa ndi kupereka Sekemu ngati gawo la cholowa.+
Ndipo ndidzayezera anthu anga chigwa cha Sukoti.+
7 Giliyadi ndi wanga ndipo Manase ndi wanganso.+
Efuraimu ndi malo otetezeka a mtsogoleri amene ine ndamuika.
Yuda ndi ndodo ya mtsogoleri wanga.+
8 Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+
Ndidzaponyera Edomu nsapato zanga.+
Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+
9 Ndani adzandibweretsa kumzinda wozunguliridwa ndi adani?+
Ndani adzanditsogolera mpaka kukafika ku Edomu?+
10 Ndinu Mulungu amene mungatichititse kupambana! Koma onani tsopano mwatitaya,+
Ndipo inu Mulungu wathu, simukupita kunkhondo pamodzi ndi magulu athu ankhondo.+