Aefeso
3 Pa chifukwa chimenechi, ine Paulo, ndine wandende+ mwa Khristu Yesu m’malo mwa inu, anthu a mitundu ina+ . . . 2 Ndithudi munamva kuti ndinaikidwa kukhala woyang’anira+ kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kuti ndikuthandizeni, 3 ndiponso kuti anandiululira chinsinsi chopatulika,+ monga ndalemba kale mwachidule. 4 Pa chifukwa chimenechi, inuyo mukawerenga zimenezi mutha kuzindikira kuti chinsinsi chopatulika+ chonena za Khristu ndikuchimvetsa bwino.+ 5 M’mibadwo ina, chinsinsi+ chimenechi sichinaululidwe kwa ana a anthu mmene chaululidwira+ tsopano kwa atumwi ndi aneneri+ ake oyera mwa mzimu. 6 Chinsinsi chimenechi n’chakuti anthu a mitundu ina nawonso akhale odzalandira cholowa, ndipo akhalenso ziwalo za thupi+ ndiponso otenga nawo mbali m’lonjezo pamodzi ndi ife,+ mogwirizana ndi Khristu Yesu kudzera mwa uthenga wabwino. 7 Ndinakhala mtumiki+ wa zimenezi mogwirizana ndi mphatso yaulere ya kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene ndinapatsidwa mogwirizana ndi mmene mphamvu yake imagwirira ntchito.+
8 Kukoma mtima kwakukulu kumeneku kunapatsidwa kwa ine, munthu wochepa pondiyerekeza ndi wochepetsetsa+ wa oyera onse. Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku+ kuti ndilengeze kwa mitundu ina+ uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera+ cha Khristu, 9 ndiponso kuti ndionetse anthu mmene chinsinsi chopatulikacho+ chikuyendetsedwera.+ Kuyambira kalekale, chinsinsi chimenechi chakhala chobisika mwa —Mulungu, amene analenga zinthu zonse.+ 10 Zinakhala choncho kuti maboma ndi maulamuliro+ amene ali m’malo akumwamba adziwe tsopano mbali zambirimbiri za nzeru ya Mulungu+ kudzera mwa mpingo.+ 11 Izi n’zogwirizana ndi cholinga chamuyaya chimene iye anakhala nacho chokhudza Khristuyo,+ yemwe ndi Yesu Ambuye wathu. 12 Kudzera mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhula ndiponso njira yofikira Mulungu+ popanda kukayikira pokhala ndi chikhulupiriro mwa Yesuyo. 13 N’chifukwa chake ndikukupemphani kuti musabwerere m’mbuyo poona masautso+ angawa, amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu, pakuti akutanthauza ulemerero kwa inu.
14 Pa chifukwa chimenechi ndikupinda mawondo+ anga kwa Atate,+ 15 amene amapangitsa banja lililonse,+ kumwamba ndi padziko lapansi, kukhala ndi dzina.+ 16 Kutinso mogwirizana ndi chuma+ cha ulemerero wake, akuloleni kuti munthu wanu wamkati+ akhale wamphamvu, mwa mphamvu ya mzimu wake,+ 17 komanso kuti mwa chikhulupiriro chanu, Khristu akhale m’mitima yanu, pamodzi ndi chikondi+ chimene chiyenera kukhala pakati panu, ndiponso kuti muzike mizu+ ndi kukhala okhazikika pamaziko.+ 18 Cholinga n’chakuti, inu pamodzi ndi oyera onse muthe kudziwa bwino+ m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama,+ 19 ndiponso kuti mudziwe chikondi cha Khristu+ chimene chimaposa kudziwa zinthu zonse, kuti mudzazidwe ndi makhalidwe onse+ amene Mulungu amapereka.
20 Tsopano kwa iye amene angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza,+ malinga ndi mphamvu yake imene ikugwira ntchito+ mwa ife, 21 kwa iye kukhale ulemerero kudzera mwa mpingo ndi mwa Khristu Yesu, ku mibadwo yonse kwamuyaya.+ Ame.