Masalimo
Nyimbo ya Asafu.+
50 Wamphamvuyo,+ Yehova, Mulungu,+ walankhula+
Ndipo akuitana dziko lapansi,+
Kuchokera kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.+
2 Mulungu wawala ali ku Ziyoni,+ mzinda wokongola kwambiri.+
3 Mulungu wathu adzabwera ndipo sadzakhala chete.+
Pamaso pake pali moto wonyeketsa,+
Ndipo pamalo onse omuzungulira pali mkuntho wamphamvu.+
7 “Ndimvereni anthu anga, ndipo ine ndilankhula,+
Inu Aisiraeli, ine ndipereka umboni wotsutsana nanu.+
Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.+
8 Sindikukudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,+
Kapena chifukwa cha nsembe zanu zopsereza zathunthu zimene mumapereka kwa ine nthawi zonse.+
11 Ndikudziwa bwino zolengedwa zonse zouluka za m’mapiri,+
Ndipo magulu a nyama zakutchire ndi anga.+
12 Ngakhale nditakhala ndi njala, sindingakuuze,
13 Kodi ndiyenera kudya nyama ya ng’ombe zamphongo zonenepa,+
Kapena kumwa magazi a mbuzi zamphongo?+
14 Pereka nsembe zoyamikira kwa Mulungu,+
Ndipo pereka kwa Wam’mwambamwamba zimene walonjeza.+
15 Pa tsiku la nsautso undiitane.+
Ine ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.”+
16 Koma Mulungu adzauza woipa kuti:+
“Ndani wakupatsa udindo wofotokoza malangizo anga,+
Ndi wolankhula za pangano langa?+
18 Nthawi zonse ukaona wakuba unali kusangalala naye.+
Ndipo unali kugwirizana ndi anthu achigololo.+
19 Walekerera pakamwa pako kulankhula zinthu zoipa,+
Ndipo ukugwiritsa ntchito lilime lako kulankhula zachinyengo.+
20 Umakhala pansi ndi kunenera m’bale wako zinthu zoipa,+
Umapezera zifukwa mwana wamwamuna wa mayi ako.+
21 Wachita zinthu zonsezi, koma ine ndinakhala chete.+
Unali kuganiza kuti ine ndikhala ngati iwe.+
Ine ndidzakudzudzula,+ ndipo ndidzaika machimo ako onse poyera iwe ukuona.+