Yesaya
3 Tamverani! Ambuye woona,+ Yehova wa makamu, akuchotsa mu Yerusalemu+ ndi mu Yuda zinthu zonse zofunika pa moyo. Akuchotsa mkate, madzi,+ 2 mwamuna wamphamvu, munthu wankhondo, woweruza, mneneri,+ wowombeza, mwamuna wachikulire,+ 3 mtsogoleri wa anthu 50,+ munthu wolemekezeka kwambiri, mlangizi, katswiri wa matsenga ndi munthu wodziwa kuseweretsa njoka.+ 4 Ndidzaika anyamata kuti akhale akalonga awo ndipo anthu ankhanza adzawalamulira.+ 5 Anthu azidzalamulirana mwankhanza, ndipo munthu azidzachitira nkhanza munthu mnzake.+ Mnyamata adzaukira nkhalamba,+ ndipo wonyozeka adzaukira wolemekezeka.+ 6 Aliyense adzagwira m’bale wake m’nyumba mwa bambo ake n’kumuuza kuti: “Iwe uli ndi nsalu. Choncho ukhale wolamulira+ wathu ndipo uzilamulira mulu wa bwinjawu.” 7 Iye adzakweza mawu ake m’tsiku limenelo n’kunena kuti: “Ine sindikufuna kukhala womanga zilonda ndipo m’nyumba mwanga mulibe mkate kapena nsalu. Musandiike kuti ndikhale wolamulira anthuwa.”
8 Yerusalemu wapunthwa ndipo Yuda wagwa,+ chifukwa lilime lawo ndiponso zochita zawo n’zotsutsana ndi Yehova.+ Iwo achita zinthu zomupandukira m’maso ake olemekezeka.+ 9 Maonekedwe a nkhope zawo akuwachitira umboni wotsutsana nawo,+ ndipo anthuwo akunena za tchimo lawo lofanana ndi la Sodomu.+ Iwo sanalibise. Tsoka kwa iwo, chifukwa adzibweretsera mavuto.+
10 Amuna inu, nenani kuti anthu olungama zidzawayendera bwino,+ chifukwa adzadya zipatso za zochita zawo.+ 11 Tsoka kwa anthu oipa! Iwo adzaona zoopsa, chifukwa zimene anachitira ena ndi manja awo, zidzawachitikira iwowo.+ 12 Amene amagawira anthu anga ntchito, akuwagwiritsa ntchito mwankhanza, ndipo akazi ndi amene akuwalamulira.+ Inu anthu anga, amene akukutsogolerani akukusocheretsani,+ ndipo asokoneza njira yanu.+
13 Yehova wakhala pamalo ake kuti afotokoze mlandu wake, ndipo waimirira kuti aweruze mitundu ya anthu.+ 14 Yehova adzaweruza achikulire pakati pa anthu ake ndi akalonga ake.+
“Inuyo mwatentha munda wa mpesa. Zinthu zimene zinabedwa kwa anthu ovutika zili m’nyumba zanu.+ 15 Kodi amuna inu mukutanthauza chiyani pophwanya anthu anga ndi kupera nkhope za anthu ovutika?”+ akutero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.
16 Yehova wati: “Ana aakazi a Ziyoni ndi odzikuza. Iwo amayenda atasolola makosi awo ndiponso amakopa amuna ndi maso awo. Amayenda modzigomera, ndipo akamayenda mapazi awo amachita phokoso chifukwa cha zokongoletsera zimene amavala m’mapazi.+ 17 Choncho Yehova adzachititsa zipere+ m’mutu mwa ana aakazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzayeretsa pamutu pawo.+ 18 M’tsiku limenelo Yehova adzachotsa zokongoletsera zawo zonse: zibangili za m’miyendo, zinthu zomanga kumutu, zodzikongoletsera zooneka ngati mwezi,+ 19 ndolo,* zibangili za m’manja, nsalu zofunda,+ 20 nsalu zovala kumutu, matcheni ovala kumiyendo, malamba a pachifuwa,+ zoikamo mafuta onunkhira,* zigoba zodzikongoletsera,+ 21 mphete zovala m’zala, mphete zovala pamphuno,+ 22 mikanjo yovala pa nthawi zapadera, malaya ovala pamwamba, mikanjo yabwino kwambiri, tizikwama, 23 magalasi oonera a m’manja,+ zovala zamkati, nduwira,*+ ndi nsalu zofunda zikuluzikulu.+
24 “Ndiyeno chidzachitike n’chakuti, m’malo mwa mafuta a basamu onunkhira+ padzangokhala fungo loipa, m’malo mwa lamba padzakhala chingwe, m’malo mwa tsitsi lokonzedwa bwino padzakhala mpala,+ m’malo mwa chovala chamtengo wapatali munthu adzavala chiguduli,*+ ndipo padzakhala chipsera*+ m’malo mwa kukongola. 25 Amuna ako adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu ako amphamvu adzaphedwa pa nkhondo.+ 26 Zipata zake zidzalira+ ndipo zidzamva chisoni. Iye adzatsala wopanda chilichonse. Adzakhala pansi, padothi penipeni.”+