Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Salimo la Asafu.
81 Anthu inu, fuulani mosangalala kwa Mulungu amene ndi mphamvu yathu,+
Fuulirani Mulungu wa Yakobo mosangalala chifukwa wapambana.+
2 Yambani kuimba nyimbo+ ndipo tengani maseche,+
Zeze womveka mosangalatsa pamodzi ndi choimbira cha zingwe.+
3 Pa tsiku lokhala mwezi, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa.+
Pa tsiku looneka mwezi wathunthu, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa, loimba pa tsiku la chikondwerero.+
5 Anaika chigamulocho monga chikumbutso kwa Yosefe,+
Pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+
Ndinali kumva chilankhulo chimene sindinali kuchidziwa.+
7 Pa nthawi ya nsautso unaitana ndipo ine ndinakupulumutsa.+
Ndinayamba kukuyankha m’malo obisika a bingu.+
Ndinakusanthula pamadzi a Meriba.+ [Seʹlah.]
8 Imvani anthu anga, ndipo ndidzakulangizani ndi kukuchenjezani.+
Zikanakhala bwino ngati mukanandimvera, inu Aisiraeli.+
10 Ine Yehova, ndine Mulungu wanu,+
Amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo.+
Tsegulani pakamwa panu ndipo ndidzaikamo chakudya.+
11 Koma anthu anga sanamvere mawu anga.+
Ndipo Isiraeli sanasonyeze kuti ndi wofunitsitsa kundimvera.+
13 Haa! Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+
Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda m’njira zanga.+