Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni.*+ Nyimbo ya Davide.
39 Ine ndinati: “Ndidzatchinjiriza njira zanga,+
Kuti ndisachimwe ndi lilime langa.+
Ndidzamanga pakamwa panga kuti patetezeke,+
Nthawi zonse pamene woipa ali pamaso panga.”+
2 Ndinakhala chete osalankhula kanthu.+
Ndinakhala phee osanena ngakhale zinthu zabwino,+
Ndipo ndinanyalanyaza ululu wanga.
4 “Inu Yehova, ndidziwitseni za kufulumira kwa chimaliziro changa,+
Ndiponso kuti masiku anga ndi ochepa motani,+
Kuti ndidziwe kufupika kwa moyo wanga.+
5 Taonani! Mwachepetsa masiku anga.+
Ndipo nthawi ya moyo wanga si kanthu pamaso panu.+
Ndithudi, munthu aliyense ngakhale atakhala wamphamvu bwanji, sali kanthu koma ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+ [Seʹlah.]
6 Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi.+
Ndithudi, anthu amapokosera pachabe.+
Munthu amaunjika zinthu ndipo sadziwa amene adzazitute.+
11 Mwa kudzudzula cholakwa, mwawongolera munthu,+
Ndipo mwawononga zinthu zake zamtengo wapatali ngati mmene njenjete*+ imachitira.
Ndithudi, munthu aliyense ali ngati mpweya.+ [Seʹlah.]