Deuteronomo
15 “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse uzilengeza kuti anthu amene anakongola zinthu zako amasuka ku ngongoleyo. 2 Kumasula anthu angongoleko kuzichitika motere:+ munthu aliyense asafunse ngongole imene anabwereketsa mnzake. Asakakamize mnzake kapena m’bale wake kupereka ngongoleyo,+ chifukwa chilengezo choti anthu angongole amasuke chiyenera kuperekedwa pamaso pa Yehova.+ 3 Mlendo+ ungam’kakamize kubweza ngongole, koma ngati m’bale wako wakongola chinthu chako chilichonse usam’kakamize kuchibweza. 4 Pakati panu pasapezeke munthu wosauka, chifukwa Yehova adzakudalitsa ndithu+ m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale cholowa chako.+ 5 Adzakudalitsa ngati udzamveradi mawu a Yehova Mulungu wako ndi kutsatiradi malamulo onsewa amene ndikukupatsa lero.+ 6 Yehova Mulungu wako adzakudalitsa ndithu monga mmene anakulonjezera ndipo mitundu yambiri idzakongola+ zinthu zako mwa kukupatsa chikole, pamene iwe sudzakongola kanthu. Udzalamulira mitundu yambiri koma mitundu sidzakulamulira.+
7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+ 8 Uzim’kongoza m’bale wako mowolowa manja,+ mulimonse mmene iye wafunira atakupatsa chikole, ndipo uzim’kongoza zimene akusowa. 9 Samala kuti usalankhule mawu achabe mumtima mwako+ kuti, ‘Chaka cha 7, chaka choti anthu angongole amasuke chayandikira,’+ kuti usaolowere manja m’bale wako wosaukayo,+ osam’patsa kalikonse. Pamenepo iye adzafuulira Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira+ ndipo udzapezeka kuti wachimwa.+ 10 Mulimonse mmene zingakhalire uzim’patsa zimene akufunazo,+ ndipo mtima wako usakhale woumira pomupatsa zinthu zimenezo, chifukwa ukakhala wowolowa manja, Yehova Mulungu wako adzakudalitsa pa chilichonse chimene ukuchita ndi pa ntchito zako zonse.+ 11 Pakuti sipadzalephera kukhala wosauka m’dziko lako.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti, ‘Uzikhala wowolowa manja kwa m’bale wako wovutika ndi wosauka m’dziko lanu.’+
12 “Ngati anakugulitsa m’bale wako, Mheberi wamwamuna kapena wamkazi,+ ndipo wakutumikira zaka 6, m’chaka cha 7 uzim’masula ndi kumulola kuchoka.+ 13 Ndipo ukam’masula ndi kumulola kuchoka, usamulole kuchoka chimanjamanja.+ 14 Uzim’patsako ndithu zina mwa nkhosa zako, mbewu zochokera pamalo ako opunthira, mafuta ochokera pamalo oyengera ndi vinyo wochokera moponderamo mphesa. Uzim’patsa malinga ndi mmene Yehova Mulungu wako wakudalitsira.+ 15 Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wako anakuwombola.+ N’chifukwa chake lero ndikukulamula zinthu zimenezi.
16 “Koma kapoloyo akakuuza kuti, ‘Ine sindikusiyani!’ chifukwa chakuti amakukonda komanso amakonda banja lako, popeza unali kukhala naye bwino,+ 17 uzitenga choboolera ndi kuboola khutu lake ali pakhomo, mpaka chobooleracho chigunde chitseko ndipo azikhala kapolo wako moyo wake wonse.+ Uzichitanso zimenezi ndi kapolo wako wamkazi. 18 Zisakhale zovuta kwa iwe kum’masula kuti achoke,+ chifukwa wakutumikira zaka 6, moti malipiro ake akanafanana ndi malipiro a anthu awiri aganyu,+ ndipo Yehova Mulungu wako wakudalitsa pa chilichonse chimene wachita.+
19 “Mwana aliyense wamphongo woyamba kubadwa wa ng’ombe kapena wa nkhosa uzim’patulira Yehova Mulungu wako.+ Usagwiritse ntchito mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe, kapena kumeta ubweya wa mwana woyamba kubadwa wa nkhosa.+ 20 Chaka ndi chaka iweyo ndi banja lako muzidya mwana woyamba kubadwa wa ng’ombe kapena wa nkhosa pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene Yehova adzasankhe.+ 21 Akakhala ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, usamam’pereke nsembe kwa Yehova Mulungu wako.+ 22 Uzimudyera mumzinda wanu ngati mmene umadyera insa ndi mbawala yamphongo.+ Nayenso munthu wodetsedwa komanso munthu woyera azidya.+ 23 Koma magazi ake okha usadye.+ Uziwathira pansi ngati madzi.+