Masalimo
2 Yehova wasonyeza mu Ziyoni kuti ndi wamkulu,+
Ndipo ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+
4 Iye amakonda chilungamo ngati mmene mfumu yamphamvu imachitira.+
Inu mwakhazikitsa kulungama.+
Mwakhazikitsa chiweruzo ndi chilungamo pakati pa ana a Yakobo.+
6 Mose ndi Aroni anali pakati pa ansembe ake,+
Samueli anali pakati pa anthu amene anali kuitana pa dzina lake.+
Iwo anali kuitana Yehova, ndipo iye anali kuwayankha.+
7 Mulungu anapitiriza kulankhula nawo mumtambo woima njo ngati chipilala.+
Iwo anasunga zikumbutso zake ndi malangizo amene anawapatsa.+