Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
75 Timakuyamikani, inu Mulungu, timakuyamikani,+
Ndipo dzina lanu lili pafupi ndi ife.+
Anthu ayenera kulengeza ntchito zanu zodabwitsa.+
2 Mulungu akuti: “Ndinasankha nthawi yoikidwiratu,+
Ndipo ndinayamba kuweruza mwachilungamo.+
3 Dziko lapansi ndi onse okhala mmenemo anayamba kusungunuka chifukwa cha mantha,+
Ndine amene ndinakonzanso zipilala zake.”+ [Seʹlah.]
4 Anthu opusa ndinawauza kuti: “Musakhale opusa,”+
Ndipo oipa ndinawauza kuti: “Musakweze nyanga.+
5 Musakweze nyanga yanu pamwamba.
Musalankhule modzikuza.+
6 Pakuti kukwezeka kwa munthu sikuchokera kum’mawa,
Kumadzulo kapena kum’mwera.
7 Mulungu ndiye woweruza.+
Amatsitsa wina ndi kukweza wina.+
8 M’dzanja la Yehova muli kapu.+
Kapuyo yadzaza ndi vinyo wosakaniza ndi zokometsera ndipo akuchita thovu.
Ndithudi, iye adzatsanula vinyo yense amene ali m’kapuyo kuphatikizapo nsenga zake.
Anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa ndi kugugudiza nsengazo.”+
9 Koma ine ndidzasimba zimenezi mpaka kalekale.
Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobo.+
10 Mulungu akuti: “Ndidzadula nyanga zonse za anthu oipa.”+
Koma nyanga za munthu wolungama zidzakwezedwa.+