2 Mafumu
21 Manase+ anali ndi zaka 12 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu. Mayi ake dzina lawo linali Hefiziba. 2 Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonyansa za mitundu+ imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli. 3 Choncho iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anachotsa.+ Anamanga maguwa ansembe a Baala n’kumanga mzati wopatulika, monga momwe Ahabu+ mfumu ya Isiraeli anachitira. Iye anayambanso kugwadira+ khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ n’kumazitumikira.+ 4 Anamanga maguwa ansembe m’nyumba ya Yehova,+ imene ponena za iyo Yehova anati: “Ku Yerusalemu ndidzaikako dzina langa.”+ 5 Iye anamangira maguwa ansembe khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ m’mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+ 6 Manase anatentha* mwana wake wamwamuna pamoto,+ ndipo ankachita zamatsenga,+ ankawombeza,*+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu ndi olosera+ zam’tsogolo. Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.
7 Komanso iye anaika m’nyumbayo chifaniziro+ cha mzati wopatulika chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo,+ Yehova anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa mpaka kalekale.+ 8 Sindidzachititsanso phazi la Isiraeli kuchoka panthaka imene ndinapatsa makolo awo,+ ngati atayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene ndinawalamula,+ ndiponso mogwirizana ndi chilamulo chonse chimene Mose mtumiki wanga anawalamula.” 9 Koma sanamvere,+ ndipo Manase anapitiriza kunyengerera anthu kuti achite zinthu zoipa+ kuposa zimene inkachita mitundu+ yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa ana a Isiraeli.
10 Yehova anapitiriza kulankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri,+ kuti: 11 “Manase+ mfumu ya Yuda yachita zinthu zonyansazi.+ Yachita zinthu zoipa kwambiri kuposa zonse zimene anachita Aamori+ amene analiko iye asanakhale mfumu. Iye wachimwitsa ngakhale Yuda+ ndi mafano ake onyansa. 12 Pa chifukwa chimenechi Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikubweretsa tsoka pa Yerusalemu+ ndi Yuda loti aliyense akamva, adzadabwa kwambiri.*+ 13 Ndithu ndidzayeza Yerusalemu ndi chingwe chimene ndinayezera+ Samariya,+ ndiponso ndidzamuyeza ndi thabwa lowongolera limene ndinayezera nyumba ya Ahabu.+ Yerusalemu ndidzam’pukuta+ mpaka kuyera mbee ngati mmene munthu amapukutira mbale yolowa mpaka kuyera mbee, n’kuitembenuza.+ 14 Ndidzataya otsala+ a cholowa changa+ n’kuwapereka m’manja mwa adani awo. Iwo adzakhala zofunkha ndipo katundu wawo adzalandidwa ndi adani awo onse.+ 15 Ndidzachita zimenezi chifukwa chakuti iwo anachita zoipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuyambira tsiku limene makolo awo anatuluka ku Iguputo mpaka lero.’”+
16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 17 Nkhani zina zokhudza Manase ndi zonse zimene anachita, ndiponso tchimo lake limene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 18 Pomalizira pake, Manase anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda m’munda wa panyumba pake, m’munda wa Uziza.+ Kenako Amoni mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.
19 Amoni+ anali ndi zaka 22 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka ziwiri+ ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Yotiba, ndipo dzina lawo linali Mesulemeti mwana wa Haruzi. 20 Amoni anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, monga anachitira Manase bambo ake.+ 21 Iye anapitiriza kuyenda m’njira zonse zimene bambo ake anayendamo,+ ndipo anapitiriza kutumikira mafano onyansa+ amene bambo ake anawatumikira, n’kumawagwadira. 22 Chotero anasiya Yehova,+ Mulungu wa makolo ake, ndipo sanayende m’njira ya Yehova.+ 23 Pomaliza pake, atumiki a mfumu Amoni anam’chitira chiwembu n’kumupha+ m’nyumba mwake momwe. 24 Koma anthu a m’dzikolo anapha anthu onse amene anachitira chiwembu+ Mfumu Amoni. Kenako anthu a m’dzikolo anaika Yosiya+ mwana wake kuti akhale mfumu m’malo mwake. 25 Nkhani zina zokhudza Amoni ndi zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 26 Chotero anamuika m’manda ake m’munda wa Uziza,+ ndipo Yosiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.