1 Mafumu
5 Hiramu+ mfumu ya ku Turo+ inatumiza atumiki+ ake kwa Solomo, pakuti inamva kuti iyeyo ndi amene anadzozedwa kulowa ufumu m’malo mwa bambo ake, popeza Hiramuyo ankamukonda Davide masiku ake onse.+ 2 Kenako Solomo anatumiza uthenga kwa Hiramu, kuti:+ 3 “Inuyo mukudziwa bwino kuti Davide bambo anga sanathe kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo+ zimene adani ake ankamenyana naye m’madera onse omuzungulira, mpaka pamene Yehova anaika adani akewo pansi pa mapazi ake. 4 Tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mpumulo pakati pa adani anga onse ondizungulira.+ Palibe amene akulimbana nane, ndipo palibe choipa chilichonse chimene chikuchitika.+ 5 Panopa ndikuganiza zomanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga,+ monga momwe Yehova analonjezera Davide bambo anga kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamuike pampando wako wachifumu m’malo mwa iweyo, ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 6 Tsopano lamulani kuti anthu andidulire mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+ Antchito anga adzakhala limodzi ndi antchito anu ndipo ndidzakupatsani malipiro a antchito anu malingana ndi zonse zomwe munganene. Inuyo mukudziwa bwino kuti pakati pathu palibenso anthu odziwa kudula mitengo ngati Asidoni.”+
7 Hiramu+ atangomva mawu a Solomo, anasangalala kwambiri ndipo ananena kuti: “Yehova atamandike+ lero, popeza wapereka kwa Davide mwana wanzeru+ woti alamulire anthu ochulukawa.”+ 8 Choncho Hiramu anatumiza uthenga kwa Solomo, kuti: “Ndamva uthenga wanu. Ineyo ndichita zonse zimene mukufuna pa nkhani ya mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza.+ 9 Antchito anga adzainyamula ku Lebanoni+ n’kutsikira nayo kunyanja, ndipo ineyo kumbali yanga ndidzaimanga pamodzi ngati phaka n’kuiyandamitsa panyanja kuti ikafike kumalo kumene mudzandiuze.+ Kenako ndidzauza anthu kuti aimasule, ndipo inuyo mukaitengera kumeneko. Ndipo inu mudzachita zofuna zanga pondipatsa chakudya cha banja langa.”+
10 Choncho Hiramu anapereka kwa Solomo mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza, monga momwe Solomo anafunira. 11 Ndipo Solomo anapereka kwa Hiramu tirigu wokwana miyezo 20,000 ya kori,*+ kuti chikhale chakudya cha banja lake, ndiponso mafuta oyenga bwino kwambiri+ okwana miyezo 20 ya kori. Izi n’zimene Solomo ankapereka kwa Hiramu chaka ndi chaka.+ 12 Ndiyeno Yehova anapatsa Solomo nzeru monga mmene anam’lonjezera.+ Pakati pa Hiramu ndi Solomo panali mtendere, ndipo awiriwa anachita pangano.
13 Anthu amene Mfumu Solomo inawalemba ntchito yokakamiza anachokera ku Isiraeli konse, ndipo anthu olembedwa ntchito yokakamizawo+ anakwana amuna 30,000. 14 Inkawatumiza ku Lebanoni m’magulu a anthu 10,000 pamwezi. Kwa mwezi umodzi anthuwo ankakhala ku Lebanoni, ndipo kwa miyezi iwiri ankakhala kwawo.+ Adoniramu+ ndiye anali woyang’anira anthu olembedwa ntchito yokakamizawo.+ 15 Solomo anali ndi anthu+ 70,000 onyamula katundu,+ ndi ena 80,000 osema miyala+ kumapiri.+ 16 Kuwonjezera pa amenewa, panalinso akapitawo a nduna za Solomo+ oyang’anira ntchitoyo. Analipo akapitawo 3,300+ oyang’anira anthu amene anali kugwira ntchitoyo. 17 Ndiyeno mfumuyo inalamula kuti aseme miyala ikuluikulu yokwera mtengo,+ kuti akamange maziko+ a nyumbayo ndi miyala yosema.+ 18 Choncho amisiri omanga a Solomo ndi amisiri omanga a Hiramu ndiponso Agebala+ anasema miyalayo, ndipo anapitiriza kudula mitengo ndi kusema miyala pokonzekera kumanga nyumbayo.