1 Akorinto
14 Yesetsani kukhala ndi chikondi, komanso pitirizani kufunafuna mwachangu mphatso zauzimu,+ makamaka kunenera.+ 2 Chifukwa wolankhula lilime lachilendo salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu, pakuti palibe amene amamva zonena zake,+ koma amalankhula zinsinsi zopatulika+ mwa mzimu. 3 Komabe, wonenera amathandiza+ anthu ndipo amawalimbikitsa ndi kuwatonthoza ndi mawu ake. 4 Wolankhula lilime lachilendo amadzilimbikitsa yekha, koma wonenera amalimbikitsa mpingo. 5 Tsopano ndikanakonda kuti nonsenu muzilankhula malilime,+ koma ndikuona kuti ndi bwino kuti muzinenera.+ Ndithudi, wonenera amaposa wolankhula malilime achilendo,+ kupatulapo ngati wa malilimeyo amasulira, kuti amange mpingo. 6 Koma pa nthawi ino abale, ngati ineyo ndingabwere kwa inu ndikulankhula malilime, kodi mungapindulepo chiyani ngati sindingakulankhuleni ndi mawu amene ndalandira kuchokera kwa Mulungu,+ kapena ndi mphatso yodziwa zinthu,+ kapena ndi ulosi, kapena ndi chiphunzitso?
7 Chabwino, zinthu zopanda moyo zimamveka kulira kwake,+ kaya chikhale chitoliro kapena zeze. Koma ngati maliridwe ake angokhala amodzi osasinthasintha, kodi n’zotheka kudziwa nyimbo imene ikuimbidwa ndi chitoliro kapena zezeyo? 8 Ndithudi, ngati lipenga likulira mwa mamvekedwe osadziwika bwino, ndani angakonzekere nkhondo?+ 9 Momwemonso, ngati simukulankhula zomveka ndi lilime lanu,+ zingatheke bwanji kudziwa zimene mukunena? Kwenikweni mudzakhala mukulankhula kwa mphepo.+ 10 Pangakhale zinenero zosiyanasiyana padziko lapansi, koma palibe zinenero zimene zilibe tanthauzo. 11 Chotero ngati sindikudziwa tanthauzo la chinenero, ndimakhala mlendo+ kwa wolankhulayo, ndipo wolankhulayo amakhala mlendo kwa ine. 12 Inunso chimodzimodzi, popeza mukufunitsitsa mphatso za mzimu.+ Chotero, yesetsani kukhala nazo zochuluka kuti mumange mpingo.+
13 Choncho amene amalankhula lilime lachilendo apemphere kuti athe kumasulira.+ 14 Pakuti ngati ndikupemphera m’lilime lachilendo, mphatso yanga ya mzimu ndi imene ikupemphera,+ koma maganizo anga amakhala opanda phindu. 15 Ndiye chofunika n’chiyani? Ndipemphere ndi mphatso ya mzimu, koma ndipempherenso ndi maganizo anga. Ndiimbe chitamando ndi mphatso ya mzimu,+ koma ndiimbenso ndi maganizo anga.+ 16 Chifukwa ngati mupereka chitamando ndi mphatso ya mzimu, kodi munthu wamba anganene bwanji “Ame”+ pa kuyamika kwanu, posadziwa zimene mukunena? 17 Zoonadi, mukupereka chiyamiko m’njira yabwino, koma munthu winayo sakulimbikitsidwa.+ 18 Ndimayamika Mulungu kuti ndimalankhula malilime ambiri kuposa nonsenu.+ 19 Ngakhale zili choncho, ndi bwino kuti mumpingo ndilankhule mawu asanu omveka, kutinso ndilangize ena ndi mawuwo, kusiyana n’kulankhula mawu 10,000 m’lilime lachilendo.+
20 Abale, musakhale ana aang’ono pa luntha la kuzindikira,+ koma khalani tiana pa zoipa,+ ndipo pa luntha la kuzindikira khalani aakulu msinkhu.+ 21 M’Chilamulo muli mawu akuti: “‘Anthu awa+ ndidzawalankhula m’malilime a alendo,+ ndipo ndidzawalankhula ndi milomo ya anthu achilendo, koma iwo sadzandimverabe,’ watero Yehova.”+ 22 Chotero malilimewo ndi chizindikiro+ kwa osakhulupirira,+ osati kwa okhulupirira, koma kunenera ndi kwa okhulupirira,+ osati osakhulupirira. 23 Ndiye chifukwa chake, ngati mpingo wonse wasonkhana malo amodzi ndipo onse akulankhula malilime,+ ndiyeno mwalowa anthu osadziwa kalikonse kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti ndinu amisala? 24 Koma ngati nonse mukunenera, ndiyeno mwalowa winawake wosakhulupirira kapena munthu wamba, iye amadzudzulidwa ndi nonsenu.+ Nonsenu mumamufufuza mosamala. 25 Zobisika za mumtima mwake zimaululika,+ moti adzagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi, n’kulambira Mulungu, ndi kunena kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.”+
26 Ndiyeno zizikhala bwanji, abale? Mukasonkhana pamodzi, wina amakhala ndi salimo, wina chiphunzitso, wina mawu amene walandira kuchokera kwa Mulungu, wina lilime lachilendo, wina kumasulira.+ Zochitika zonse zikhale zolimbikitsa.+ 27 Ndipo ngati pali anthu olankhula lilime lachilendo, asapose awiri kapena atatu, azisiyirana mpata, ndipo wina amasulire.+ 28 Koma ngati palibe womasulira, wa malilimeyo akhale chete mumpingo. Adzilankhule yekha mumtima+ ndipo alankhule kwa Mulungu. 29 Aneneri awiri kapena atatu+ alankhule, ndipo ena onse azindikire tanthauzo la zimene iwo alankhula.+ 30 Koma ngati mneneri wina amene wakhala pansi walandira mawu kuchokera kwa Mulungu,+ woyambayo akhale chete. 31 Pakuti nonse munganenere,+ koma mmodzi ndi mmodzi, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa.+ 32 Ndipo mphatso za mzimu za aneneri ziyenera kulamulidwa ndi aneneri. 33 Pakuti Mulungu si Mulungu wachisokonezo,+ koma wamtendere.+
Mofanana ndi m’mipingo yonse ya oyerawo, 34 akazi akhale chete+ m’mipingo, pakuti sikololeka kuti iwo azilankhula, koma akhale ogonjera,+ monga Chilamulo+ chimanenera. 35 Koma ngati akufuna kumvetsa chinachake, akafunse amuna awo kunyumba, popeza n’zochititsa manyazi+ kuti mkazi azilankhula mumpingo.
36 Kodi mawu a Mulungu anachokera kwa inu,+ kapena anafika kwa inu nokha?
37 Ngati munthu akuganiza kuti ndi mneneri kapena ali ndi mphatso ya mzimu, avomereze zimene ndakulemberanizi, chifukwa ndizo lamulo la Ambuye.+ 38 Koma ngati wina savomereza, akhale. 39 Choncho abale anga, pitirizani kufunafuna mwakhama uneneri,+ komanso musaletse kulankhula malilime.+ 40 Koma zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.+