Masikili. Salimo ndiponso pemphero la Davide, pamene anali kukhala kuphanga.+
142 Ndinafuulira Yehova kuti andithandize.+
Ndinafuulira Yehova kuti andikomere mtima.+
2 Ndinapitirizabe kumukhuthulira nkhawa zanga.+
Ndinapitirizabe kumuuza masautso anga.+
3 Ndinachita zimenezi pamene mtima wanga+ unalefuka.
Pamenepo, munadziwa njira yanga.+
Adani anga anditchera msampha+
M’njira imene ndikuyenda.+
4 Yang’anani kudzanja lamanja ndipo muone
Kuti palibe aliyense amene akufuna kundithandiza.+
Ndilibenso malo othawirako,+
Ndipo palibe amene akufunsa za moyo wanga.+
5 Ndinafuula kwa inu kuti mundithandize, inu Yehova.+
Ndinanena kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga,+
Gawo langa+ m’dziko la amoyo.”+
6 Mvetserani kulira kwanga kochonderera,+
Pakuti ndasautsika koopsa.+
Ndipulumutseni kwa anthu amene akundizunza,+
Pakuti iwo ndi amphamvu kuposa ine.+
7 Nditulutseni mundende ya mdima+
Kuti nditamande dzina lanu.+
Chititsani kuti anthu olungama asonkhane ndi kundizungulira,+
Chifukwa mumandichitira zabwino.+