Yesaya
59 Dzanja la Yehova silinafupike moti n’kulephera kupulumutsa,+ komanso khutu lake silinagonthe moti n’kulephera kumva.+ 2 Ayi si choncho. Koma zolakwa za anthu inu n’zimene zakulekanitsani ndi Mulungu wanu,+ ndipo machimo anu amuchititsa kuti akubisireni nkhope yake, kuti asamve zimene mukunena.+ 3 Pakuti m’manja mwanu mwaipitsidwa ndi magazi,+ ndipo zala zanu zaipitsidwa ndi zolakwa.+ Milomo yanu yanena zabodza. Lilime lanu limangokhalira kunena zinthu zopanda chilungamo.+ 4 Palibe amene akufuula mwachilungamo,+ ndipo palibe amene amalankhula mokhulupirika akapita kukhoti. Anthu inu mukukhulupirira zinthu zachabechabe+ ndipo mukulankhula zopanda pake.+ Mwatenga pakati pa mavuto ndipo mwabereka zopweteka.+
5 Iwo aikira mazira a njoka yapoizoni, ndipo ankangokhalira kuluka ukonde wa kangaude.+ Aliyense wodya mazira a njoka yapoizoniyo amafa, ndipo dzira limene laswedwa limaswa mphiri.+ 6 Ukonde wawo wa kangaude sudzakhala chovala chawo, ndipo iwo sadzavala zochita zawo.+ Ntchito zawo n’zopweteka ena, ndipo m’manja mwawo muli ntchito zachiwawa.+ 7 Mapazi awo amangothamangira kukachita zoipa,+ ndipo amafulumira kuti akakhetse magazi osalakwa.+ Maganizo awo ndi opweteka anzawo.+ M’misewu mwawo amangokhalira kusakazana ndi kuwonongana.+ 8 Iwo amangonyalanyaza njira yamtendere,+ ndipo m’njira zawo mulibe chilungamo.+ Misewu yawo aikhotetsakhotetsa.+ Palibe munthu aliyense woyenda mmenemo amene adzadziwe mtendere.+
9 N’chifukwa chake chilungamo chatitalikira kwambiri, ndipo zolungama sizikutipeza. Tinali kuyembekezera kuunika koma m’malomwake tikungoona mdima. Tinali kuyembekezera kuwala koma tikungoyendabe mu mdima wosatha.+ 10 Tikungoyenda ndi khoma ngati anthu akhungu, ndipo tikungofufuzafufuza ngati anthu opanda maso.+ Tapunthwa masanasana ngati kuti tili mu mdima wamadzulo. Pakati pa anthu ojintcha, tikungokhala ngati anthu akufa.+ 11 Tonsefe tikungolira ngati zimbalangondo ndipo tikungokhalira kubuula momvetsa chisoni ngati njiwa.+ Tinali kuyembekezera chilungamo+ koma sichinabwere. Tinali kuyembekezera chipulumutso koma chakhala nafe kutali.+ 12 Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso panu,+ ndipo tchimo lathu lililonse likupereka umboni wotsutsana nafe.+ Pakuti zolakwa zathu zili pa ife, ndipo zochimwa zathu tikuzidziwa bwino.+ 13 Ife taphwanya malamulo ndipo tamukana Yehova.+ Tabwerera m’mbuyo n’kumusiya Mulungu wathu. Tanena zinthu zopondereza ena ndi zopanduka.+ Taganiza mawu achinyengo mumtima mwathu n’kumawalankhula chapansipansi.+ 14 Chilungamo tinachikankhira m’mbuyo,+ ndipo chilungamocho chinakangoima patali.+ Pakuti choonadi chapunthwa ngakhale m’bwalo la mumzinda, ndipo zinthu zolungama zikulephera kulowamo.+ 15 Choonadi chikusowa+ ndipo aliyense wokana zoipa akusakazidwa.+
Yehova anaona zimenezi ndipo zinamuipira m’maso mwake poona kuti panalibe chilungamo.+ 16 Iye ataona kuti panalibe munthu aliyense woti n’kuthandizapo, anadabwa kwambiri poona kuti palibe amene akulowererapo.+ Chotero anapulumutsa anthu ndi dzanja lake, ndipo chilungamo chake n’chimene chinamulimbikitsa kuchita zimenezo.+ 17 Choncho iye anavala chilungamo monga chovala chodzitetezera chamamba achitsulo,+ ndiponso anavala chisoti cholimba chachipulumutso kumutu kwake.+ Kuwonjezera apo, anavala chilungamo monga chovala kuti akapereke chilango kwa adani ake+ ndiponso kuchita zinthu modzipereka kwambiri kunali ngati chovala chake chodula manja.+ 18 Iye adzawapatsa mphoto mogwirizana ndi zochita zawo.+ Adani ake adzawapatsa mkwiyo ndipo anthu otsutsana naye adzawapatsa chilango chowayenerera.+ Zilumbanso adzazipatsa chilango choyenerera.+ 19 Amene ali kolowera dzuwa adzayamba kuopa dzina la Yehova,+ ndipo amene ali kotulukira dzuwa adzaopa ulemerero wake.+ Pakuti iye adzabwera ngati mtsinje woyambitsa mavuto woyendetsedwa ndi mzimu wa Yehova.+
20 “Wowombolayo+ adzabwera ku Ziyoni+ ndiponso kwa mbadwa za Yakobo zimene zasiya zolakwa zawo,”+ akutero Yehova.
21 Yehova wanena kuti: “Koma pangano langa ndi iwowo+ ndi ili:
“Mzimu wanga umene uli pa iwe+ ndi mawu anga amene ndaika m’kamwa mwako,+ sizidzachoka m’kamwa mwako ndiponso m’kamwa mwa ana ako kapenanso m’kamwa mwa ana a ana ako, kuyambira panopa mpaka kalekale,” watero Yehova.+