Levitiko
3 “‘Ngati akupereka nsembe yachiyanjano+ kwa Yehova, ndipo akufuna kupereka ng’ombe yamphongo kapena yaikazi, azipereka yopanda chilema.+ 2 Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu+ pa ng’ombeyo, ndipo aziipha pakhomo la chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni, ansembe, aziwaza magazi ake mozungulira paguwa lansembe. 3 Pamenepo azipereka mbali ina ya nsembe yachiyanjanoyo monga nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. Azipereka mafuta+ okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo.+ 4 Aziperekanso impso ziwiri+ ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi,* aziwachotsa pamodzi ndi impsozo. 5 Kenako ana a Aroni+ azitentha+ zinthu zimenezi paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza yomwe ili pankhuni+ zimene zili pamoto. Imeneyi ikhale nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi+ kwa Yehova.
6 “‘Ngati akupereka nkhosa kapena mbuzi monga nsembe yachiyanjano kwa Yehova, azipereka yamphongo kapena yaikazi, yopanda chilema.+ 7 Ngati akupereka nkhosa yaing’ono yamphongo monga nsembe yake, aziipereka kwa Yehova.+ 8 Pamenepo aziika dzanja lake pamutu+ pa nkhosayo, ndipo aziipha+ patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero, ana a Aroni aziwaza magazi ake mozungulira guwa lansembe. 9 Ndipo pansembe yachiyanjanoyo azitengapo mafuta ake ndi kuwapereka kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto.+ Azichotsa mchira wonse wamafuta+ pafupi ndi fupa la msana ndiponso mafuta okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo.+ 10 Azichotsanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta+ a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo. 11 Ndipo wansembe azitentha+ zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya,+ kuti chikhale nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.
12 “‘Ngati akupereka mbuzi+ monga nsembe yake, aziibweretsa pamaso pa Yehova. 13 Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu pa mbuziyo,+ ndipo aziipha+ patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni, aziwaza magazi ake mozungulira guwa lansembe. 14 Ndipo pambuziyo azitengapo mafuta okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo,+ ndi kuwapereka kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto. 15 Aziperekanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo. 16 Ndipo wansembe azitentha zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi. Mafuta onse ndi a Yehova.+
17 “‘Musamadye mafuta kapena magazi+ alionse. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale,* kulikonse kumene mungakhale.’”