Masalimo
Salimo la Davide.
35 Weruzani mlandu wanga inu Yehova, motsutsana ndi adani anga.+
Menyani nkhondo ndi kugonjetsa amene akumenyana ndi ine.+
2 Tengani chishango chaching’ono ndi chishango chachikulu,+
Ndipo bwerani kuti mundithandize.+
3 Tengani mkondo ndi nkhwangwa ya pankhondo kuti mukumane ndi anthu amene akundilondalonda.+
Uzani moyo wanga kuti: “Ine ndine chipulumutso chako.”+
4 Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi ndi kunyozeka.+
Amene akundikonzera chiwembu muwabweze ndipo athedwe nzeru.+
7 Iwo andikumbira mbuna popanda chifukwa ndi kuikapo ukonde,+
Akumba mbunazo kuti ndigweremo ngakhale kuti sindinalakwe.+
8 Awonongeke pamene iwo sakuyembekezera,+
Akodwe mu ukonde umene atchera okha.+
Agweremo ndi kuwonongeka.+
10 Ndinene ndi mtima wanga wonse kuti:+
“Inu Yehova, ndani angafanane ndi inu,+
Amene mumalanditsa wosautsika m’manja mwa munthu wamphamvu kuposa iyeyo,+
Amene mumalanditsa wozunzika ndi wosauka m’manja mwa munthu amene akumulanda zinthu zake?”+
13 Iwo akadwala ndinali kuvala chiguduli,+
Ndinali kusautsa moyo wanga mwa kusala kudya.+
Ndipo mapemphero anga anali kubwerera kwa ine osayankhidwa.+
14 Chifukwa cha mnzanga ndiponso m’bale wanga,+
Ndinamva chisoni kwambiri ngati munthu wolira maliro a mayi ake.+
Ndinawerama chifukwa cha chisoni.
15 Atandiona ndikuyenda motsimphina anasangalala ndipo anasonkhana pamodzi.+
Anasonkhana pamodzi kuti alimbane nane.+
Anandimenya pamene sindinali kuyembekezera.+
Anandikhadzulakhadzula ndipo sanakhale chete.+
17 Inu Yehova, kodi mudzayang’anira zimenezi kufikira liti?+
Ndipulumutseni kwa anthu ofuna kundiwononga,+
Pulumutsani moyo wanga+ ku mikango yamphamvu.
19 Musalole kuti anthu amene amadana ndi ine popanda chifukwa akondwere ndi kusautsika kwanga.+
Ndipo musalole kuti anthu amene amandida popanda chifukwa anditsinzinire diso.+
20 Iwo salankhula mawu amtendere,+
Koma amakonzera chiwembu anthu ofatsa a padziko lapansi,
Kuti awachitire zachinyengo.+
23 Nyamukani ndi kukhala maso kuti mundichitire chilungamo,+
Chitani zimenezi inu Mulungu wanga Yehova, kuti muweruze mlandu wanga.+
24 Inu Yehova Mulungu wanga, mundiweruze mogwirizana ndi chilungamo chanu,+
Musalole kuti adani anga akondwere ndi kusautsika kwanga.+
25 Musalole kuti mumtima mwawo anene kuti: “Eya! Izi ndi zimene timafuna.”+
Ndipo asanene kuti: “Tamumeza.”+
26 Onse amene akukondwera ndi tsoka langa,+
Achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+
Onse odzikweza pamaso panga achite manyazi+ ndi kutsitsidwa.+