Masalimo
95 Bwerani tifuule kwa Yehova mokondwera!+
Iye amene ndi Thanthwe la chipulumutso chathu, timufuulire mosangalala chifukwa wapambana.+
2 Tiyeni tionekere pamaso pake ndi chiyamiko.+
Tiyeni tiimbe nyimbo zomutamanda ndi kumufuulira mosangalala chifukwa wapambana.+
3 Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,+
Ndiponso ndi Mfumu yaikulu kuposa milungu ina yonse.+
4 Malo ozama kwambiri a dziko lapansi ali m’manja mwake,+
Mapiri aatali nawonso ndi ake.+
5 Nyanja imene anapanga ndi yake,+
Iye amenenso anapanga mtunda ndi manja ake.+
7 Pakuti iye ndi Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu ake. Iye amatisamalira ngati nkhosa zimene akuweta.+
Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+
8 Musaumitse mitima yanu monga mmene makolo anu anachitira pa Meriba,+
Monga mmene anachitira pa Masa m’chipululu,+
9 Pamene makolo anu anandiyesa.+
Iwo anandisanthula, ndipo anaonanso ntchito zanga.+