Tito
2 Koma iwe pitiriza kulankhula zinthu zogwirizana ndi chiphunzitso cholondola.+ 2 Amuna achikulire+ akhale osachita zinthu mopitirira malire, opanda chibwana,+ oganiza bwino, achikhulupiriro cholimba,+ achikondi chachikulu, ndi opirira+ kwambiri. 3 Chimodzimodzinso akazi achikulire.+ Akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche,+ kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino, 4 kuti azikumbutsa akazi achitsikana kukonda amuna+ awo, kukonda ana+ awo, 5 kukhala oganiza bwino, oyera,+ ogwira ntchito zapakhomo, abwino ndi ogonjera+ amuna awo, kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.+
6 Mofanana ndi zimenezi, pitiriza kulimbikitsa anyamata kuti akhale oganiza bwino.+ 7 M’zinthu zonse, ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino.+ Chiphunzitso+ chako chikhale chopanda chinyengo.+ Usonyeze kuti ndiwe wopanda chibwana. 8 Mawu ako akhale oyenera amene sangatsutsike,+ kuti munthu wotsutsa achite manyazi, ndipo asapeze choipa chotinenera nacho.+ 9 Akapolo+ azigonjera ambuye awo pa zonse+ ndipo aziwakondweretsa. Asamatsutsane nawo+ 10 kapena kuwabera,+ koma akhale okhulupirika pa chilichonse,+ kuti akometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi+ wathu Mulungu, m’zinthu zonse.
11 Pakuti Mulungu waonetsa+ kukoma mtima kwake kwakukulu+ kumene kumabweretsa chipulumutso+ kwa anthu, kaya akhale a mtundu wotani.+ 12 Zimenezi zatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu+ ndi zilakolako za dziko,+ koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu+ m’nthawi* ino.+ 13 Tizichita zimenezi pamene tikuyembekeza kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo+ chosangalatsa ndi kuonetsedwa kwaulemerero+ kwa Mulungu wamkuluyo ndiponso kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. 14 Iyeyo anadzipereka+ m’malo mwa ife kuti atilanditse+ ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse,+ kuti tikhale anthu akeake,+ odzipereka pa ntchito zabwino.+
15 Pitiriza kulankhula zimenezi, kulimbikitsa ndi kudzudzula anthu mogwirizana ndi ulamuliro wonse umene wapatsidwa.+ Munthu aliyense asakuderere.+