31 Makolo athu anadya mana mʼchipululu,+ monga mmene Malemba amanenera kuti: ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”+ 32 Kenako Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Mose sanakupatseni chakudya chochokera kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba.