Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 16:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Mame aja atauma, panthaka yamʼchipululumo panapezeka tinthu topyapyala ndi tolimba koma tosalala+ ngati madzi amene aundana panthaka.

  • Ekisodo 16:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Aisiraeli anadya mana kwa zaka 40+ mpaka pamene analowa mʼdziko limene munkakhala anthu.+ Iwo ankadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a dziko la Kanani.+

  • Ekisodo 16:31, 32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Nyumba ya Isiraeli inapatsa chakudyacho dzina lakuti “mana.”* Chinali choyera ngati mapira,* ndipo kukoma kwake kunali ngati makeke opyapyala othira uchi.+ 32 Kenako Mose anati: “Yehova walamula kuti, ‘Dzazani muyezo umodzi wa omeri ndi mana kuti asungidwe mʼmibadwo yanu yonse,+ nʼcholinga choti iwo adzaone chakudya chimene ndinakupatsani mʼchipululu nditakutulutsani mʼdziko la Iguputo.’”

  • Numeri 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Manawo+ anali ngati mapira,*+ ndipo ankaoneka ngati utomoni woonekera mkati ngati galasi.

  • Deuteronomo 8:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Anakuphunzitsani kudzichepetsa pokulolani kuti mukhale ndi njala+ nʼkukudyetsani mana,+ amene inu kapena makolo anu sankawadziwa. Anachita zimenezi kuti mudziwe kuti munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.+

  • Yohane 6:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Makolo athu anadya mana mʼchipululu,+ monga mmene Malemba amanenera kuti: ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”+

  • 1 Akorinto 10:2, 3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Onse anabatizidwa mwa Mose, kudzera mu mtambo ndi nyanja. 3 Onse ankadya chakudya chauzimu chofanana.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena