Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 19:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Musamadye chilichonse chimene chili ndi magazi.+

      Musamaombeze kapena kuchita zamatsenga.+

  • Levitiko 20:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Munthu amene wachita zosakhulupirika* podalira anthu olankhulana ndi mizimu+ komanso olosera zamʼtsogolo,+ ndidzadana naye ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+

  • Deuteronomo 18:10-12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakati panu pasapezeke munthu wowotcha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ aliyense wochita zamatsenga,+ aliyense woombeza,+ wanyanga,+ 11 aliyense wochesula* ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu+ kapena wolosera zamʼtsogolo,+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+ 12 Chifukwa aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wanu akuwathamangitsa pamaso panu.

  • 1 Samueli 28:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pa nthawiyi nʼkuti Samueli atamwalira ndipo Aisiraeli anali atalira maliro ake nʼkumuika mʼmanda mumzinda wakwawo wa Rama.+ Komanso Sauli anali atachotsa mʼdzikolo anthu olankhula ndi mizimu ndiponso olosera zamʼtsogolo.+

  • Agalatiya 5:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 kulambira mafano, kukhulupirira mizimu,*+ chidani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko,

  • Chivumbulutso 22:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu* komanso amene amachita zamizimu, achiwerewere,* opha anthu, olambira mafano ndi aliyense amene amakonda kunama komanso kuchita zachinyengo.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena