-
Deuteronomo 18:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pakati panu pasapezeke munthu wowotcha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ aliyense wochita zamatsenga,+ aliyense woombeza,+ wanyanga,+ 11 aliyense wochesula* ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu+ kapena wolosera zamʼtsogolo,+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+ 12 Chifukwa aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wanu akuwathamangitsa pamaso panu.
-